Puberty in girls

Puberty in girls

Puberty is a sequence of events in which physical changes occur, resulting in adult physical characteristics and capacity to reproduce. When a girl is growing up there a lot of things that changes within her body. Some of the changes include development of breast, hair growing under arms and in the pubic area, skin changes, including pimples for some girls and an increase in height among others. Most girls experience these changes from the ages of 9, 10 and 11 but some may take a bit longer to experience these changes.

There are so many reasons why some girls will experience these changes early and others late and this does not mean that one has a problem but some of the things that may delay changes during puberty are genes of a particular person, food and the environment she lives in.

When girls see that they are delaying to experience these changes than their friends they feel like maybe they have a problem but the truth is people are different and they grow differently at their own time.

When a girl has become of age she starts developing sexual feelings and this is the time that she should be more aware of family planning methods to avoid getting pregnant at a tender age as well as sexually transmitted diseases including HIV.

If you have questions on growing up and the changes that one experiences when growing up, call Tithandizane Helpline Toll free line- 116 or you can visit your nearest youth friendly health facility or YONECO Drop In Centers.

Kutha msinkhu kwa mtsikana

Pa nthawi imene mtsikana watha msinkhu, pamakhala zambiri zomwe zimasintha mnthupi lake. Zina mwa zinthuzi ndi monga, kuyamba kusamba kapena kuti piriyodi, kukula mabere, kumela tsisti ku maliseche, kuyamba ziphuphu, kukula mahipi ndi zina. Atsikana ambiri amatha msinkhu akafika zaka 9, 10, 11 ndipo ena amachedwerapo kuti athe msinkhu nkuyamba kuona zizindikilo zatchulidwa zija.

Pali zifukwa zosiyanasiyana zomwe zimapangitsa kuti atsikanan ena athe msinkhu mofulumira ndipo ena achedwelepo. Mtsikana akachedwa kutha msinkhu sizikutanthauza kuti ali ndi ulumali. Zinthu zomwe zimachitsa kuti mtsikana athe msinkhu mwansanga kapena mochedwerapo ndi monga izi; chibadwa chabe, zakudya zomwe amadya, nyengo ya komwe akukhala komanso zomwe munthu amakonda kuchita.

Atsikana ambiri akaona kapena kunva anzawo akukamba nkhani zokhudza zomwe amaona akatha msinthu amaona ngati iwowo ali ndi vuto. Chilungamo pa nkhaniyi ndichokuti anthu ndi osiyana ndipo kakulidwe kamakhalanso kosiyana. Ngakhale izi zili choncho, pakantha nthawi aliyense amatha msikhu ndipo sikulumara.

Pa nthawi imene mntsikana watha msikhu amakhalanso ndi chilakolako chofuna kuchita zogonana. Imeneyi ndinthawi yomwe mntsikana akuyenera kudziwa bwino nkhani zokhudza uchembere ndi ubeleki. Kupanda kutero, pamakhala chiopsezo chokuti akhoza kutenga mimba mosayembekezera ngakhalenso matenda opatsirana pogonana kuphatikizapo kachiromo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a EDZI.

Atsikana ambiri amakhala okhumudwa pa nkhani yokhudza makulidwe awo ndipo nkoyenera kunvetsetsa bwino mmene zimakhalira. Mtsikana akhoza kunva zambiri zokhudza kuntha msinkhu pokafunsa ku chipatala komwe kuli thanzizo la umoyo lokomera achinyamata, kuyimba foni mwaulere Tithandizane Helpline pa 116 komanso kupita kumalo okumanirako achinyata a YONECO.

CHICHEWA

Author: YONECO

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *