Managing Peer Pressure

Managing Peer Pressure

Peer pressure is when an individual does things just to fit in with friends, and this includes changing one’s behavior, dressing and other things just to be part of a grouping. This happens most when one is growing up especially among young people and this tends to affect young people’s lives in different ways whether good or bad not depending on age or whether one is a girl or a boy.

Peer pressure comes with different reasons and some of these are lack of communication between parents and children, seeking validation from friends and peers and failure to distinguish between bad and good.

Influence from peers is mostly the common peer pressure among young people and mostly they force each other to experience drinking beer or smoking marijuana to seem elite to fellow peers. It is therefore important that you should open up with your parents, teachers or your guardians to verify the information that you get from friends to avoid making wrong choices.

You can call Tithandizane Helpline toll free line 116 for more information on managing peer pressure or visit your nearest YONECO Drop in Centre

Kukopeka-kuyipa ndi ubwino wake

kukopeka kapena kuti peer pressure ndipamene munthu akuchita zinthu pofuna kufanana ndi anzake ofanana nawo msinkhu. Izi ndikuphatikizapo kusintha khalidwe komanso zochita zako pofuna kuti uthe kukhala mugulu limodzi ndi anzako.  Kutengeka ndi mbali imodzi ya moyo wamunthu yomwe amadutsamo akamakula ndipo kumachitika kwambiri pakati paachinyamata. Kutengekaku kumakhudza umoyo wa   wachinyamata munjira zosiyana siyana zomwe ndi zabwino komanso zoyipa posatengera zaka zake komanso kuti ndiwammuna kapena wamkazi. Zotsatira zakutengekaku zimatengera kukhwima nzeru kwa wachinyamatayu kapena msinkhu waku. Kutengekaku kumadza kaamba kakusakambirana pakati pamakolo ndi ana awo, kufuna kuvomerezedwa mugulu la anzathu komanso kulephera kusiyanitsa pakati pachabwino ndi choyipa. Kutengekaku kumadza munjira zosiyanasiyana, nthawi zina anzathu amatikakamiza kuchita zikhalidwe zina monga kusuta chamba, kumwa mowa ndicholinga choti mudzioneka ozindikira. Nthawi zina  wachinyamata amatengeka posakakamizidwa kudzera nkuyankhula koma poona anzake akuchita zikhalidwe zina ndipo iye amafuna kudziyenereza potsatira zomwe iwo akuchita zinthu zomwe zimamuyika mmavuto. Ngakhale kutengekaku kuli ndi zotsatira zoyipa paumoyo wachinyamata, pali kutengeka kwina komwe kumathandiza achinyamata kuchita zisankho zabwino mmoyo mwawo. Mwachitsanzo achinyamata ena anasiya kupanga zikhalidwe zoyipa monga kumwa mowa kapena kusuta chamba pofuna kuchita zinthu zomwe zingawapindulire moyo wawo ngati kulimbikira maphunziro awo potengera anzawo ena omwe akuchita bwino pamaphunziro awo. Ngati wachinyamata ukuyenera   kusamalitsa popanga zisankho  zamoyo wako ndikupewa kutengeka pa zomwe anzako akuchita.

Pofuna kumva zambiri momwe mungapangire zisankho zoyenera zomwe zingakuthandizeni kukwaniritsa maloto anu imbani phone  mwaulele patithandizane helpline 116 kupita ku youth club yomwe ili mdera lanu kapena malo okumanirana achinyamata kuma drop  in centres a YONECO.

CHICHEWA

Author: YONECO

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *